2 Samuel 23:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nati, “Ndithudi pali Chauta, sindingachite chinthu chotere, chifukwa kukhala ngati kumwa magazi a anthuŵa amene adaika moyo wao paminga.” Motero adakana kumwa madziwo. Zimenezi ndizo adachita anthu atatu amphamvu aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati, Ndisachite ichi ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa anapitawa ndi kutaya moyo wao? Chifukwa chake iye anakana kumwa. Izi anazichita ngwazi zitatuzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Inu Yehova, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi awa si magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Ndipo Davide sanamwe madziwo. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati, Ndisacite ici ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa ana pitawa ndi kutaya moyo wao? Cifukwa cace iye anakana kumwa. Izi anazicita ngwazi zitatuzi.