2 Samuel 23:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo anali womveka kwambiri mwa atsogoleri makumi atatu aja, ndipo adasanduka mkulu wao. Komabe sadafikepo pa anthu atatu aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? Chifukwa chake anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikana ndi atatu oyamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi iyeyo sanali wolemekezeka koposa? Iye anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti sanali mʼgulu la anthu atatu aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? cifukwa cace anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikana ndi atatu oyamba.