2 Samuel 23:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Benaya mwana wa Yehoyada, wa ku Kabizeele, anali munthu wolimba mtima amene ankachita ntchito zamphamvu. Iyeyo adapha ankhondo aŵiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina chisanu cha mbee chitagwa, adatsikira m'chitsime, naphamo mkango.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabzeli amene anacita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Moabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya cipale cofewa;