2 Samuel 23:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaphanso Mwejipito wina, wa maonekedwe okongola. Mwejipitoyo adaali ndi mkondo m'manja, koma Benaya adapita kwa iyeyo ndi ndodo chabe. Adalanda mkondowo ku manja mwa Mwejipito uja, namupha ndi mkondo wake womwewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m'dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye anakanthanso Mwigupto wamkulu msinkhu. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anapha M-aigupto munthu wokongola, M-aigupto anali nao mkondo m'dzanja lace; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wa iye mwini.