2 Samuel 23:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu wa Israele walankhula, Thanthwe la Israele landiwuza kuti, ‘Munthu amene amalamulira anthu mwachilungamo, kuŵalamulira molemekeza Mulungu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu wa Israeli anayankhula, Thanthwe la Israeli linati kwa ine: ‘Pamene munthu alamulira anthu mwachilungamo, pamene alamulira moopa Mulungu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu wa Israyeli anati, Thanthwe la Israyeli Gnalankhula ndi ine; Kudzakhala woweruza anthu molungama; Woweruza m'kuopa Mulungu.