2 Samuel 23:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
amaŵafikira ngati kuŵala kwam'maŵa amaŵaŵalira ngati dzuŵa lam'maŵa pa tsiku lamitambo. Alinso ngati mvula imene imameretsa udzu pa nthaka.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, potuluka dzuwa, M'mawa mopanda mitambo; pamene msipu uphuka kutuluka pansi, chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
amakhala ngati kuwala kwa mmamawa, mmawa wopanda mitambo, monga kuwala pamene mvula yaleka kugwa imene imameretsa udzu mʼnthaka.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, poturuka dzuwa, M'mawa mopanda mitambo; Pamene msipu uphuka kuturuka pansi, Cifukwa ca kuwala koyera, italeka mvula.