2 Samuel 23:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Mulungu adzadalitsa zidzukulu zanga chifukwa Iye adachita nane chipangano chosatha, chipangano cholongosoka bwino ndi chosasinthika. Izi nzimene ndikulakalaka, ndiponso zimene zidzandipulumutsa. Ndi Mulungu amene adzachita zonsezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha, lolongosoka mwa zonse ndi losungika; pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse, ndi kufuma kwanga konse, kodi sadzachimeretsa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi banja langa silolungama pamaso pa Mulungu? Kodi Iye sanachite pangano losatha ndi ine, lokonzedwa ndi lotetezedwa mbali zonse? Kodi sadzakwaniritsa chipulumutso changa, ndi kundipatsa chokhumba changa chilichonse?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; Koma iye anapangana ndi ine pangano losatha, Lolongosoka mwa zonse ndi losungika; Pakuti ici ndi cipulumutso canga conse, ndi kufuma kwanga konse, Kodi sadzacimeretsa?