2 Samuel 23:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa maina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti, wa ku Takemoni, mkulu wa atsogoleri ankhondo atatu. Iye adaamenyana nkhondo ndi anthu 800, naŵapha onsewo ndi mkondo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Yosebu-Basebeti Mtakemoni, mkulu wa akazembe; ameneyu ndiye Adino Mwezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti wa ku Takemoni mkulu wa atsogoleri a ankhondo atatu. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 800 nthawi imodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Josebu-basebete Mtakemoni, mkuru wa akazembe; ameneyu ndiye Adino M-ezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.