2 Samuel 23:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mnzake wotsatana naye mwa anthu atatu amphamvu aja anali Eleazara, mwana wa Dodo, mwana wa Aho. Iyeyo anali pamodzi ndi Davide pamene ankaputa Afilisti omwe adaasonkhana kuti amenyane naye nkhondo ku Pasi-Damimu. Aisraele anali atathaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi. Monga mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu a Davide, iye anali ndi Davide pamene anazunza Afilisti amene anasonkhana ku Pasi-Damimu kuchita nkhondo. Kenaka ankhondo a Israeli anabwerera mʼmbuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wotsatana naye Eleazeri mwana wa Dodai mwana wa M-akohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atacoka Aisrayeli;