2 Samuel 24:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Davide adadzitsutsa mumtima mwake, atatha kaundulayo. Ndipo adapemphera kwa Chauta kuti, “Ndachimwa kwambiri pochita zimenezi. Koma tsopano, Inu Chauta, ndikukupemphani kuti mundikhululukire tchimo langa ine mtumiki wanu, popeza kuti ndachita zopusa kwambiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwo. Davide nati kwa Yehova, Ndinachimwa kwakukulu ndi chinthu chimene ndinachita; koma tsopano Yehova muchotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinachita kopusa ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anatsutsika mu mtima mwake atatha kuwerenga anthuwo ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono Yehova, ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwoo Davide nati kwa Yehova, Ndinacimwa kwakukuru ndi cinthu cimene ndinacita; koma tsopano Yehova mucotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinacita kopusa ndithu.