2 Samuel 24:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Gadi adadza kwa Davide, namuuza kuti, “Musankhe, kodi pabwere zaka zitatu zanjala m'dziko mwanu, kapena inu mukhale mukuthaŵa adani anu pa miyezi itatu, kapena pakhale mliri wa masiku atatu m'dziko mwanu? Ganizani bwino, ndipo mutsimikize chilichonse choti muyankhe, kuti ine ndikauze amene adanditumayo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupirikitsani miyezi itatu? Kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Chenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa iye, “Kodi mungakonde kuti mʼdziko mwanu mukhale njala kwa zaka zitatu? Kapena kuti mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu? Kapena kuti mʼdziko muno mukhale mliri kwa masiku atatu? Tsopano, ganizirani bwino ndipo musankhe chomwe mudzamuyankhe amene wandituma.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Gadi anafika kwa Davide, namuuza, nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupitikitsani miyezi itatu? kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Cenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.