2 Samuel 24:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Davide adauza Gadi kuti, “Iyai, ine pamenepa ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka tigwe m'manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu. Koma chonde, tisagwe m'manja mwa anthu ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ife atilange ndi Yehova pakuti chifundo chake ndi chachikulu, koma ndisalangidwe ndi anthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zace nzazikuru; koma tisagwe m'dzanja la munthu.