2 Samuel 24:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Chauta adagwetsa mliri pa Aisraele, kuyambira m'maŵa mpaka pa nthaŵi imene adaafuna mwini wake, mwakuti kuchokera ku Dani mpaka ku Beereseba adafa anthu okwanira 70,000 pamodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikira; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, kuyambira mmawa mpaka pa nthawi imene anafuna mwini wake, ndipo unapha anthu 70,000 kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Yehova anatumiza mliri pa Israyeli kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.