2 Samuel 24:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo pamene mngelo adatambalitsa dzanja lake kuloza mzinda wa Yerusalemu kuti auwononge, Chauta adasintha maganizo achilangowo, nauza mngelo wake amene ankaononga anthu uja kuti, “Iyai, basi tsopano! Kwakwanira. Bweza dzanja lakolo.” Nthaŵi imeneyo nkuti mngelo wa Chautayo ataima pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lake ku Yerusalemu kuuononga, choipacho chinachititsa Yehova chisoni, Iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Myebusi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mngelo anatambasula dzanja lake kuti awononge Yerusalemu, Yehova anamva chisoni chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lace ku Yerusalemu kuuononga, coipaco cinacititsa Yehova cisoni, iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Mjebusi.