2 Samuel 24:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adaona mngelo uja, ndipo adalankhula ndi Chauta, nati, “Ndachimwa ndine, ndipo ndachita choipa. Koma nkhosa izi kodi zachita chiyani? Amangonditsatira chabe. Tsono dzanja lanu likanthe ine ndi banja la bambo wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide ataona mngelo amene ankakantha anthu uja, anati kwa Yehova, “Ine ndi amene ndachimwa. Ine mʼbusa ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Langani ineyo pamodzi ndi banja langa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndacimwa ine, ndinacita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinacitanji? dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.