2 Samuel 24:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho mfumu Davide adauza Yowabu ndi atsogoleri ankhondo amene anali naye pamodzi kuti, “Pitani pakati pa mafuko onse a Aisraele kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, mukaŵerenge anthu kuti ndidziŵe chiŵerengero chao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inanena ndi Yowabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israele, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kuchuluka kwao kwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mfumu inati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali nawo. “Pitani pakati pa mafuko onse a Israeli kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba kuti mukawerenge anthu omenya nkhondo ndi cholinga choti ndidziwe chiwerengero chawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inanena ndi Yoabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israyeli, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kucuruka kwao kwa anthu.