2 Samuel 24:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Arauna atapenya chakunsi, adaona mfumu ikudza kwa iye pamodzi ndi atumiki ake. Pomwepo Araunayo adapita kukalambira mfumu choŵerama pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Arauna atayangʼana ndi kuona mfumu ndi anthu ake akubwera kumene kunali iye, iyeyo anatuluka ndi kuwerama pamaso pa mfumu mpaka nkhope yake kugunda pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ace alikubwera kwa iye; naturuka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yace pansi.