2 Samuel 24:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adafunsa mfumu kuti, “Bwanji mbuyanga mfumu, mukudza kwa ine mtumiki wanu?” Davide adati, “Ndikufuna kuti ndigule malo opunthira tirigu aja, kuti ndimangirepo Chauta guwa, kuti mliriwu uŵachoke anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Arauna nati, Mbuye wanga mfumu, mwadzeranji kwa mnyamata wanu? Ndipo Davide, anati, Kugula dwale lako ili, kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe, kuti mliriwo ulekeke kwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Arauna anati, “Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mfumu mwabwera kwa mtumiki wanu?” Davide anayankha kuti, “Kudzagula malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe kuti mliri uli pa anthuwa usiye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Arauna nati, Mbuye wanga mfumu, mwadzeranji kwa mnyamata wanu? Ndipo Davide anati, Kugula dwale lako gi, kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe, kuti mliriwo ulekeke kwa anthu.