2 Samuel 24:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo kumeneko adamangako guwa, kumangira Chauta, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Choncho Chauta adamva kupemba kwake kopembera dziko, ndipo mliriwo udaleka m'dziko la Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Ndipo Yehova anayankha pempherolo mʼmalo mwa dziko lonse, ndipo mliri unatha pa Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka cifukwa ca dziko, ndi mliri wa pa Israyeli unalekeka.