2 Samuel 24:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yowabu adauza mfumu kuti, “Chauta Mulungu wanu achulukitse anthu makumi khumi kupambana m'mene alirimu, ndipo alole kuti inu mbuyanga mfumu mudzaziwone zimenezo. Koma chifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mukufuna chinthu chotere?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yowabu anayankha mfumu kuti, “Yehova Mulungu wanu achulukitse ankhondo anu kukhala miyandamiyanda, ndipo alole inu mbuye wanga mfumu mudzazione zimenezi. Koma nʼchifukwa chiyani inu mbuye wanga mfumu mukufuna kuchita zimenezi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwacurukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu acione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi cinthu ici?