2 Samuel 24:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe mau a mfumu adapambana mau a Yowabu ndi a atsogoleri ankhondo aja. Choncho Yowabu ndi atsogoleri ankhondowo adachokapo kuti akaŵerenge Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu ndi atsogoleri a ankhondo. Choncho anachoka pamaso pa mfumu kupita kukawerenga anthu omenya nkhondo mu Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mau a mfumu anapambana Yoabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yoabu ndi atsogoleri a khamulo anaturuka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israyeli.