2 Samuel 24:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adakafika ku linga la Tiro ndi ku mizinda yonse ya Ahivi, ndi ya Akanani. Atatero, adachoka kumeneko nakafika kumwera kwa Yuda, ku Beereseba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nafika ku linga la Tiro ndi kumidzi yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; natulukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iwo anapita molunjika linga la ku Turo ndi ku mizinda yonse ya Ahivi ndi Akanaani. Pomaliza anapita ku Beeriseba ku Negevi wa ku Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nafika ku linga la Turo ndi ku midzi yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; naturukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.