2 Samuel 3:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachotsa ufumu pa banja la Saulo ndi kuupereka kwa Davide, kuti alamulire Israele ndi Yuda kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuchotsa ufumu kunyumba ya Saulo ndi kukhazika mpando wachifumu wa Davide pa Israele ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazikitsa ufumu wa Davide pa Aisraeli onse ndi Yuda kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kucotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazika mpando wadfumu wa Davide pa Israyeli ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.