2 Samuel 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abinere adatuma amithenga kwa Davide ku Hebroni kukamufunsa kuti, “Kodi dzikoli nlayani? Tipangane, ine ndidzakuthandizani kuti dziko la Israele likhale lanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abinere anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? Natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisraele onse atsate inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Abineri anatuma amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Kodi dzikoli ndi la yani? Uchite mgwirizano ndi ine ndipo ndidzakuthandiza kuti Aisraeli onse azikutsatira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abineri anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisrayeli onse atsate inu.