2 Samuel 3:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Davide adati, “Chabwino, tipangana. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: sudzandiwona ukapanda kubwera ndi Mikala, mwana wamkazi wa Saulo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anati, “Chabwino. Ine ndichita mgwirizano ndi iwe. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: Usabwere pamaso panga pokhapokha utabweretsa Mikala mwana wamkazi wa Sauli, ukamabwera kudzandiona.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Cabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira cinthu cimodzi, ndico kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Sauli, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.