2 Samuel 3:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mwamuna wakeyo adamtsatira mkaziyo. Mwamunayo ankapita nalira njira yonse mpaka ku Bahurimu. Abinere adamuuza kuti, “Iwe, bwerera.” Iye uja nkubwereradi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwamuna wakeyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Bahurimu. Pomwepo Abinere ananena naye, Choka, bwerera; ndipo anabwerera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mwamuna wake anapita naye akulira pambuyo pake njira yonse mpaka ku Bahurimu. Kenaka Abineri anati kwa iye, “Bwerera kwanu!” Ndipo anabwerera kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwamuna waceyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Baburimu. Pomwepo Abineri ananena naye, Coka, bwerera; ndipo anabwerera.