2 Samuel 3:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye zimenezi muchitedi. Paja Chauta adalonjeza Davide kuti, ‘Ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele kwa Afilisti kudzera mwa iwe mtumiki wanga, ndipo ndidzaŵapulumutsa kwa adani ao onse.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chitani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano chitani zimenezo! Pakuti Yehova analonjeza Davide kuti, ‘Kudzera mwa mtumiki wanga Davide ndidzapulumutsa anthu anga Aisraeli mʼdzanja la Afilisti ndi kuwachotsa mʼmanja mwa adani awo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
citani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, a Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisrayeli ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse.