2 Samuel 3:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abinere adauza Davide kuti, “Loleni ndikasonkhanitse Aisraele onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuyanga mfumu, kuti adzachite nanu chipangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Choncho Davide adamlola Abinere kuti apite. Ndipo iye adapita mwamtendere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Abinere anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisraele onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Chomwecho Davide analawirana ndi Abinere, namuka iye mumtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Abineri anawuza Davide kuti, “Loleni kuti ndipite msanga kukasonkhanitsa Aisraeli onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuye wanga mfumu, kuti adzachite nanu pangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Kotero Davide analola Abineri kuti apite, ndipo anapita mwamtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Abined anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisrayeli onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Comweco Davide analawirana ndi Abineri, namuka iye mumtendere.