2 Samuel 3:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yomweyo ankhondo a Davide adafika ndi Yowabu kuchokera kumene adaakamenya nkhondo, atatenga zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ndi Davide ku Hebroni, popeza kuti anali atamlola kuti apite, ndipo iye anali atapitadi mwamtendere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yowabu anabwera kuchokera ku nkhondo yovumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ku Hebroni kwa Davide, chifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo ankhondo a Davide ndi Yowabu anafika kuchokera kumene anakathira nkhondo ndipo anabweretsa katundu wambiri wolanda ku nkhondo. Koma Abineri sanalinso ndi Davide ku Hebroni, chifukwa Davide anamulola kuti apite, ndipo anapita mu mtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yoabu anabwera kucokera ku nkhondo yobvumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abineri sanali ku Hebroni kwa Davide, cifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.