2 Samuel 3:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yowabu ndi ankhondo onse amene anali nawo adabwera, ena adauza Yowabuyo kuti, “Abinere mwana wa Nere adaabwera kwa amfumu, ndipo amfumuwo adamlola kuti apite, mwakuti wapitadi mwamtendere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono pofika Yowabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yowabu nati, Abinere mwana wa Nere anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu ndi asilikali onse amene anali naye atafika, anawuzidwa kuti Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu ndipo kuti mfumu yamulola kuti apite ndi kuti wapita ndi mtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono pofika Yoabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yoabu nati, Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendereo