2 Samuel 3:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu amfumu, monga Abinere, mwana wa Nere, simumdziŵa? Amene ujatu adaabwera kudzangokumyatani m'maso. Adaafuna kudzangokutambwani, kuti adziŵe zonse zimene mukuchita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mumdziwa Abinere mwana wa Nere kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kutuluka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikuchita inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mukumudziwa bwino Abineri mwana wa Neri. Iye anabwera kudzakunamizani ndi kudzaona mayendedwe anu ndiponso kudzaona zonse zimene mukuchita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mumdziwa Abineri mwana wa Neri kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kuturuka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikucita inu.