2 Samuel 3:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Abinere ankabwerera ku Hebroni, Yowabu adamtengera pambali, pafupi ndi chipata, nakhala ngati afuna kulankhula naye poduka mphepo. Pomwepo Yowabu adabaya Abinere m'mimba, nkuferatu. Yowabu adachita zimenezi chifukwa choti Abinere anali atamuphera mbale wake Asahele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Abineri atabwerera ku Hebroni, Yowabu anamutengera pambali ku chipata, kukhala ngati akufuna kuyankhula naye mwamseri. Ndipo kumeneko pobwezera imfa ya mʼbale wake Asaheli, Yowabu analasa iyeyo mʼmimba, ndipo anafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pofikanso Abineri ku Hebroni, Yoabu anampambutsa kupita nave pakati pa cipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, cifukwa ca mwazi wa Asaheli mbale wace.