2 Samuel 3:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlandu umenewu ugwere Yowabu ndi onse a pa banja la bambo wake. Ndipo Mulungu amlange Yowabuyu kuti pabanja pake pasadzakhale popanda munthu wa nthenda ya chidzonono, kapena wakhate, kapena wolumala, kapena wophedwa ku nkhondo kapenanso wosoŵa chakudya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chilango chigwere pa mutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlandu umenewu ukhala pa Yowabu ndi banja lonse la abambo ake! Mʼbanja la Yowabu musadzasowe munthu wodwala matenda a chizonono kapena khate, kapena wolumala woyendera ndodo kapena wophedwa ndi lupanga, kapena wosowa chakudya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cilango cigwere pa mutu wa Yoabu ndi pa nyumba yonse ya atate wace; ndipo kusasoweke ku nyumba ya Yoabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa cakudya.