2 Samuel 3:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adauza Yowabu ndi anthu onse amene anali naye kuti, “Ng'ambani zovala zanu, muvale ziguduli, kuti mulire maliro a Abinere.” Ndipo mfumu Davide mwiniwake ankatsatira onyamula mtembowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zovala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'chuuno, nimulire Abinere. Ndipo mfumu Davide anatsata chithatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi anthu onse amene anali nawo, “Ngʼambani zovala zanu ndipo muvale ziguduli, muyende mukulira patsogolo pa Abineri.” Mfumu Davide mwini anayenda motsatira chitandacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zobvala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'cuuno, nimulire Abineri. Ndipo mfumu Davide anatsata cithatha.