2 Samuel 3:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakamuika Abinere ku Hebroni. Ndiye mfumu idalira mokweza mau ku manda a Abinere. Nawonso anthu onse adalira kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika Abinere ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ake nilira ku manda a Abinere, nalira anthu onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anamuyika Abineri mʼmanda ku Hebroni ndipo mfumu inalira mokweza pa manda a Abineri. Ndipo anthu onse analiranso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika Abineri ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ace nilira ku manda a Abineri, nalira anthu onse.