2 Samuel 3:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka anthuwo adadza kudzapempha mfumu kuti adye chakudya kudakali koyera. Koma Davide adalumbira kuti, “Mulungu andilange kwabasi, ngati ndidya chakudya kapena kanthu kena kalikonse dzuŵa lisanaloŵe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide chakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka onse anabwera kwa Davide kumuwumiriza kuti adye kusanade. Koma Davide analumbira kuti, “Mulungu andilange ine, andilange kwambiri, ngati ndilawe buledi kapena chilichonse dzuwa lisanalowe!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide cakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.