2 Samuel 3:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ine lero ndafooka kwambiri, ngakhale kuti ndine mfumu yodzozedwa. Ndithu anthu ameneŵa, ana aamuna a Zeruya, akundivutitsa kwambiri. Chauta abwezere munthu wochita zoipa molingana ndi kuipa kwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo amuna awa ana a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo lero, ngakhale ine ndine mfumu yodzozedwa, ndilibe mphamvu ndipo ana awa a Zeruya ndi amphamvu kwa ine. Yehova abwezere woyipa molingana ndi zoyipa zake!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndikali wofoka ine lero, cinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo amuna awa ana a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wocita coipa monga mwa coipa cace.