2 Samuel 3:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa, mwana wa Aya. Tsono Isiboseti adafunsa Abinere kuti, “Chifukwa chiyani wakaloŵa kwa mzikazi wa bambo wanga?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo adali ndi mkazi wamng'ono, dzina lake ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abinere, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng'ono wa atate wanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa mwana wa Ayiwa. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, “Nʼchifukwa chiyani unagona ndi mzikazi wa abambo anga?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli adali ndi mkazi wamng'ono, dzina lace ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng'ono wa atate wanga?