2 Samuel 4:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamene wina adaandiwuza kuti Saulo wamwalira, naganiza kuti wabwera ndi uthenga wabwino, ine ndidamgwira, ndipo ndidamupha ku Zikilagi. Imeneyo idaali mphotho yomwe adalandira chifukwa cha uthenga wakewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
muja munthu wina anandiuza kuti, Onani Saulo wamwalira, ndi kulingalira kuti alikubwera nao uthenga wabwino, ndinamgwira ndi kumupha ku Zikilagi, ndiyo mphotho yake ndinampatsa chifukwa cha uthenga wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamene munthu wina anandiwuza kuti, ‘Sauli wafa’ ndipo ankaganiza kuti wabweretsa nkhani yabwino, ine ndinamugwira ndi kumupha ku Zikilagi. Iyi inali mphotho imene ndinapereka kwa iyeyo chifukwa cha uthenga wake!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
muja munthu wina anandiuza kuti, Onani Sauli wamwalira, ndi kulingalira kuti alikubwera nao uthenga wabwino, ndinamgwira ndi kumupha ku Zikilaga, ndiyo mphotho yace ndinampatsa cifukwa ca uthenga wace.