2 Samuel 4:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga nanji anthu oipa amene adapha munthu wopanda chifukwa ali gone m'nyumba mwake, kodi ndingapande kukulangani chifukwa cha imfa ya munthuyo, mpaka kukuchotsani pa dziko lapansi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wake m'nyumba yakeyake, ndidzafunsira mwazi wake ku dzanja lanu tsopano, ndi kukuchotsani ku dziko lapansi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nanji pamene anthu oyipa apha munthu wosalakwa ali mʼnyumba mwake ndiponso pa bedi lake! Kodi ine ndingaleke kukulangani ndi kukuchotsani pa dziko lapansi pano?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wace m'nyumba yace yace, ndidzafunsira mwazi wace ku dzanja lanu tsopano, ndi kukucotsani ku dziko lapansi?