2 Samuel 4:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Davide adalamula ankhondo ake, ndipo adaŵapha anthuwo, naŵadula manja ndi mapazi, naŵapachika pambali pa dziŵe la ku Hebroni. Koma adatenga mutu wa Isiboseti, nakauika m'manda a Abinere ku Hebroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide analamulira anyamata ake, iwo nawapha, nawapachika m'mbali mwa thamanda ku Hebroni atawadula manja ndi mapazi ao. Koma mutu wa Isiboseti anautenga nauika m'manda a Abinere ku Hebroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Davide analamulira ankhondo ake, ndipo anawapha. Iwo anawadula manja ndi mapazi ndi kupachika matupi awo pa dziwe la ku Hebroni. Koma anatenga mutu wa Isi-Boseti nawuyika mʼmanda a Abineri ku Hebroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide analamulira anyamata ace, iwo nawapha, nawapacika m'mbali mwa thamanda ku Hebroni atawadula manja ndi mapazi ao. Koma mutu wa Isiboseti anautenga nauika m'manda a Abineri ku Hebroni.