2 Samuel 4:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Isibosetiyo anali ndi anthu aŵiri amene anali atsogoleri a magulu ankhondo. Wina anali Baana, wina anali Rekabu, onsewo ana a Rimoni, wa fuko la Benjamini, wa ku Beeroti (pakuti Beeroti ndi chigawo cha Benjamini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Isiboseti anali ndi anthu akuluakulu awiri amene ankatsogolera magulu a ankhondo. Mmodzi mwa iwo dzina lake linali Baana ndipo mnzakeyo anali Rekabu. Iwo anali ana a Rimoni wa banja la Beeroti wa fuko la Benjamini Beeroti. Iwo ankatengedwa ngati mbali imodzi ya Benjamini,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Isiboseti, mwana wa Sauli anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lace Baana, ndi dzina la mnzace ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;