2 Samuel 4:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Rekabu ndi Baana, ana aja a Rimoni Mbeerotiŵa, adanyamuka. Masana dzuŵa likuswa mtengo, adakafika ku nyumba ya Isiboseti, nthaŵi imene iyeyo anali pa mpumulo wamasana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika kunyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti ananyamuka kupita ku nyumba ya Isi-Boseti, ndipo anafika nthawi ya masana kukutentha pamene iye amapumula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika ku nyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana.