2 Samuel 4:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aŵiriwo ataloŵa m'nyumbamo, adampeza Isibosetiyo ali gone pabedi pake. Iwo aja adambaya nkumupha, namdula mutu. Adanyamula mutuwo, nayenda nawo usiku wonse kudzera njira ya ku Araba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali chigonere pakama pake m'chipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wake, nautenga namuka njira ya kuchidikha usiku wonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo analowa mʼnyumbamo iye akugona pa bedi mʼchipinda chake. Atamulasa ndi kumupha, anadula mutu wake nʼkuwutenga, nayenda usiku wonse mʼnjira yopita ku Araba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali cigonere pakama pace m'cipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wace, nautenga namuka njira ya kucidikha usiku wonse,