2 Samuel 4:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mutu wa Isibosetiwo adapita nawo kwa Davide ku Hebroni. Adauza mfumuyo kuti, “Amfumu, suwu mutu wa Isiboseti, mwana wa Saulo, mdani wanu uja ankafunafuna kukuphaniyu. Lero lino Chauta walipsirira Saulo ndi zidzukulu zake chifukwa cha inu mbuyanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwera nao mutu wa Isiboseti kwa Davide ku Hebroni, nanena ndi mfumu, Taonani mutu wa Isiboseti mwana wa Saulo, mdani wanu amene anafuna moyo wanu; Yehova anabwezerera chilango mbuye wanga mfumu lero lino kwa Saulo ndi mbeu yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anabweretsa mutu wa Isi-Boseti kwa Davide ku Hebroni ndipo anati kwa mfumu, “Nawu mutu wa Isiboseti mwana wa Sauli, mdani wanu, amene anafuna kukuphani. Lero lino Yehova wabwezera mbuye wanga mfumu adani anu, Sauli ndi ana ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwera nao mutu wa Isiboseti kwa Davide ku Hebroni, nanena ndi mfumu, Taonani mutu wa Isiboseti mwana wa Sauli, mdani wanu amene anafuna moyo wanu; Yehova anabwezerera cilango mbuye wanga mfumu lero lino kwa Sauli ndi mbeu yace.