2 Samuel 5:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adatuma amithenga kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza, ndiponso amisiri a matabwa ndi ena odziŵa kumanga ndi miyala. Iwowo adadzamangira Davide nyumba yachifumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Hiramu mfumu ya Turo inatumiza amithenga ake kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndi amisiri a matabwa ndi amisiri a miyala, ndipo anamumangira Davide nyumba yaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hiramu mfumu ya Turo anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.