2 Samuel 5:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu yolamulira dziko la Aisraele, adapita kukamfunafuna. Koma Davide atamva zimenezo, adatsikira ku linga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israele, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anachimva natsikira kungaka kuja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anakalowa mu linga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israyeli, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anacimva natsikira kungaka kuja.