2 Samuel 5:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo nkubwera nawonso. Ndipo Chauta adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Aisraele, udzakhala mfumu ya Israele.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kale lija, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova anakuwuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku anapitawo, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisrayeli kuturuka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israyeli, ndi kukhala mtsogoleri wa Israyeli,