2 Samuel 5:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Davide adapita ku Baala-Perazimu, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kumeneko. Tsono adati, “Ine ndikufika, Chauta waŵang'amba pakati adani anga ngati madzi a chigumula.” Nchifukwa chake malo amenewo amatchedwa kuti Baala-Perazimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anafika ku Baala-Perazimu, nawakantha kumeneko Davideyo; nati, Yehova wathyola adani anga pamaso panga ngati madzi okamulira. Chifukwa chake analitcha dzina la malowo Baala-Perazimu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Davide anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Yehova waphwanya adani anga ine ndikuona.” Choncho anawatcha malowa Baala Perazimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anafika ku Baalaperazimu, nawakantha kumeneko Davideyo; nati, Yehova wathyola adani anga pamaso panga ngati madzi okamulira. Cifukwa cace analicha dzina la malowo Baalaperazimu.