2 Samuel 5:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide atafunsa Chauta, adamuyankha kuti, “Usakaŵathire nkhondo kumaso. Uŵadzere cha kumbuyo, uŵathire nkhondo pa malo oyang'anana ndi mitengo ya mkandankhuku ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Davide anafunsira kwa Yehova, Iye anati, Usamuke, koma ukawazungulire kumbuyo kuti ukawatulukire pandunji pa mkandankhuku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anafunsa Yehova ndipo Yehovayo anayankha kuti, “Usapite molunjika koma uzungulire kumbuyo kwawo ndipo ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Davide anafunsira kwa Yehova, iye anati, Usamuke, koma ukawazungulire kumbuyo kuti ukawaturukire pandunji pa mkandankhuku.